Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 170

Miyambi ya Patsokwe Mwana akalilira nyanga ya nsatsi, m’semere im’fotere yekha kumanja. -Munthu akamafuna zinthu zopanda pake ndi bwino kumusiya kuti awone yekha zotsatira zake. Zimenezi zingamuthandize kuti amvetse chifukwa chake mumamukaniza ndipo sanga- dzabwerezenso. Mwana amalira ndi mkodzo wake womwe. -Anthu achibwana amachita zinthu zomwe pambuyo pake amadzanong’oneza nazo bondo n’kumafuna kuti ena awathan- dize. Mwana amaopa kachirombo kakamuluma. -Kuti munthu adziwe kuti chinthuchi n’choopsa, amaphunzira akakumana ndi mavuto. Mwana amene amasamba m’manja amadya ndi akuluakulu. -Mwana wakhalidwe amapeza zabwino komanso amakondedwa ndi akuluakulu. Mwana m’nyanja alimbikira mpani wake. -Munthu aliyense amalimbikira kuchita zinthu zake. Amaonet- setsa kuti zachitika bwino kwambiri koposa mmene akanachitira za ena. Mawuwa amanenedwanso munthu akamachita zinthu zokondera pa mlandu wa m’bale wake. Mwana ndi bango, akafa amaphuka wina. -Mawuwa amanenedwa potonthoza makolo omwe mwana wawo wamwalira kuti asadandaule Mulungu adzawapatsa wina. Mwana sakulira nakubala. -Ngakhale mwana ataphunzira bwanji kapena atakula chamtun- du wanji, ayenera kumalemekezabe makolo ake. Angachite zim- enezi ngakhale zitakhala kuti aliyense amamulemekeza 169