Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 9
Matigari
tsopano ndipo magazi awo akangosakanikirana ndi dothi,
ankakhala asilikali okonzeka kumenya nkhondo yolimbana ndi
atsamunda.*
*Zimene zafotokozedwazi zinkachitika pachinamwali pomwe anthu ankaimba nyimbo komanso
kuvina mwambo wa mdulidwe ukamachitika. Zimenezi zingaimirenso zimene anthu
anakumana nazo nkhondo yolimbana ndi atsamunda isanachitike.
Maganizowa atamuchoka, anaimirira n'kuyang'ana kumene
anakwirira zida zake kuja, ndipo anayamba kudziyankhulira
yekha mong’ung’udza kuti, “Zili bwino tsopano kuti ndakwirira
zida zanga.” Ndiyeno anadula khungwa lamtengo wina
n'kulimanga m'chiuno mwake. Kenako anang’ung’udzanso kuti,
“Ndadzimanga ndi lamba wamtendere. Tsopano ndipite kwathu
kuti ndikamangenso nyumba yanga.” Kenako anawoloka
mtsinje uja n’kutuluka m’nkhalango.
8