Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 8
Matigari
Ndiyeno anatenga AK47 ija n'kuikulunga ndi mapepala
apulasitiki ndipo ngati dzira, anaiika mosamala m'dzenje lija.
Kenako anapita kukatsuka chikandalanga chija kumtsinje.
Atamaliza anachisomeka m'chimake n’kukachiika m’dzenje
anaika mfuti lija.
M'chiuno mwake anali atavala lamba wokongoletsedwa ndi
mikanda yofiira, yabuluu komanso yobiriwira. Palambayu
mpamene ankakolekapo mfuti yake ina ya pistole. Ndiyeno
anayamba kumasula lambayo mokhala ngati sakufuna,
anawerenga zipolopolo, kenako anapinda lamba uja n'kuika
zonse m'dzenje muja. Atamaliza anayang'ana zinthuzo kwa
kanthawi mokhala ngati akuzitsanzika ndipo kenako
anazikwirira ndi dothi. Asanachoke anavindikira pamalowo ndi
masamba ouma ndipo anaonetsetsa kuti wafufuta madindo a
mapazi ake komanso chilichonse chomwe chikanachititsa
munthu kuzindikira kuti pamalopo pabisidwa zinthu.
Kenako ananyamuka n'kupita kumtsinje kuja kukasukusula.
Madziwo ankazizira zedi ndipo anamukumbutsa makedzana,
pa nthawi yomwe anali kuchisimba kumtsinje wina.
Anakumbukira zomwe zinkachitika pa nthawi yachinamwali
chawo, pomwe ankaimba nyimbo usiku wonse ali panja, kunja
kukulavula mphepo yoluma. Ankaimba kuti:
Kunjaku kukanachaa,
Kunjaku kukanachaa,
n'kadapita kukasamba madzi ozizira limodzi ndi mbalame zam'mawa.
Madzi ozizira moyerekedwawo ankawachititsa dzanzi moti
sankamva kupweteka ngakhale anamkungwi ankacheka
khungu lawo ndi lumo. Pa nthawiyo anali adakali anyamata
achisodzera, koma zinkachitika kuti akangomaliza mwambowu,
anyamatawo ankasanduka ana aamuna. Ankakhala akula
7