Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 7
Matigari
Mtsamunda Williams anali atatsikira kuli chete, ndipo
sankakayikira mpang’ono pomwe zoti walandilidwa ndi manja
awiri ku Gahena monga malipiro a kuipa mtima kwake.
Tsopano dzuwa n’kuti likuthamangira paliwombo, komabe
kunja kunali ngululu moti sankatha kuona patali. Iye anali
wamtali komanso wojintcha ndipo ngakhale kuti mavuto a
ukalamba anali asanamunjate, ankaoneka wachikulire ndithu
chifukwa n’kuti kumutu kwake kutachita phulusa. Anali atavala
chipewa chakhonde, chomwe chingwe chake anachimanga
pachigama. Chipewachi chinali chikongoletsedwa ndi kansalu
kokhala ndi mikanda yamitundumitundu. Anavalanso chijasi
chachikopa cha kambuku, chomwe chinali chitasosokasosoka.
Chijasicho chinkamulekeza m'mawondo. Magambusi omwe
anavala ankaoneka kuti akumana nazo chifukwa anali
atazolowerana bwino ndi chisongole ndipo n'kuti ali
ming’ankhaming’ankha.
Akuyenda m'mbali mwa mtsinje uja, anaona mtengo umene
ankaufunafuna. Unali mtengo waukulu wamkuyu womwe unali
pakati pa chikanga china. Mtengowo unkaoneka bwinobwino
chifukwa unali waukulu kuposa mitengo yonse pachikangapo
ndipo ngakhale mitsitsi yake inayi, yomwe inali itatumbula
nthaka, inkaoneka bwinobwino ukakhala patali. Umodzi mwa
mitsitsiyo unali pakati ndipo inayo inali m'mbali. Atafika
pamtengopo, anaika pansi mfuti yake ija moitsamiritsa
kumtengowo kwinaku akumwetulira ndipo anasolola
chikandalanga chake chomwe ankachibisa m'chijasi chija.
Kenako anayamba kukumba pansi pafupi ndi m’tsitsi wapakati
uja. Atamaliza, anatenga masamba ouma n'kuwaika pansi pa
dzenje anakumbalo.
6