Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 6
Matigari
Gawo 1
M'dzanja lake lamanja munali mfuti ya AK47. Dzuwa n'kuti
likukwera ndipo kuti lisamulowe m’maso, ankagwiritsa ntchito
dzanja lake lamanzere popherera cheza chake. Pa nthawiyi
n’kuti ali m’mbali mwa mtsinje ndipo tsidya lina la mtsinjewo
ndi lomwe linakola chidwi chake. Aka sikanali koyamba kuchita
zangati zimenezi. Kwa zilumika zosawerengeka, ankadutsa
akujodimajodima m'mapiri komanso m’zigwa za m’derali,
ndipo anali atazungulira ngodya zonse za dziko lapansi.
Nkhondo inali itafika kumapeto tsopano. Komabe, ankadziwa
kuti akufunika kumagona diso limodzi lili lotsegula.
Posakhalitsa hatchi ina inadutsa chapafupi ili jidimujidimu.
Hatchiyo inaima, n'kumuyang'ana kwa kanthawi ngati
ikumudziwa. Kenako inalowa m'zikanga n'kuzimiririka.
Hatchiyo inamukumbutsa Mtsamunda Williams komanso
anzake omwe ankakonda kukwera mahatchi akamapita
kokashomola nkhandwe, agalu awo onenepa ali tawatawa
kuwatsatira. Zimenezi zinachititsa kuti maganizo ake abwerere
padzana.
Mtsamunda ameneyu anali ndi ludzu la magazi osati
pang'ono! Nthawi zambiri ankakonda kuvala zofiira,
n'kutengana ndi anzake kupita kukasaka ali pamsana
pamahatchi. Munthu woyambirira kupha nkhandwe ankaidula
mchira akusangalala, ndipo ankakadzodza magazi ake
pamphumi pa mkazi wake. Ndithu, panalidi patadutsa zaka
zambiri asanaonenso zangati zimenezi zikuchitika.
Akakumbukira nthawiyo, iye ankavomereza kuti mdima
ungakule, usiku ungatalike bwanji, koma kunja kumacha basi!
Iye ankakhulupirira kuti mavuto onse omwe ankabwera
chifukwa cha ulamuliro wachitsamunda atha tsopano.
5