Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 10
Matigari
Gawo 2
Anayenda wa Adamu kuchoka kunkhalango kuja ndipo
anadutsa zigwa komanso mapiri ambirimbiri. Ankayenda
mwamphamvu m’tchire komanso m’zipululu ndipo kenako
anayamba kupeza minda. Iye anayendabe molunjika
pamchombo penipeni pa dzikolo. Tsopano n’kuti dzuwa
likuswa mtengo moti anavula chijasi chake chija n’kuchikoleka
paphewa lake lamanja, ndipo anaponya phazi mwana
wamwamuna. Dzuwa linkamuwomba m’maso, koma iye
sanabwerere m’mbuyo kapena kuima. Zovala zake zinali
zitakokolola zisoso ndipo zinkangokhala ngati zisosozo
zikumuchingamira pochoka kunkhalango kuja. Apa n’kuti ali
thukuta kamukamu, kunja kunkatentha osati pang’ono komanso
kunali fumbi osati sewero. Munthudi amafunika kupirira
mayesero ambiri akamayenda ulendo wa moyo padzikoli.
Ngakhale anatopa, ankadziwa kuti sangakafike kumene akupita
akapanda kusuntha phazi.
Pamene ankayenda ankangoganizira za kwawo. M’maganizo
mwake ankaona maheji komanso minda yodzadza ndi zokolola.
Apa n’kuti atatsala pang’ono kufika ndipo ankakwera mtunda
wotsiriza kuti akafike kumene anachoka, kunyumba yawo
yomwe inali pamwamba pa phiri.
Miyendo inali itayamba kumulemera moti anaganiza zoti
aphe kaye mpola. Anaika pansi chijasi chake chija ndipo
anakhala pamthunzi atatsamira mtengo. Kenako anachotsa
chisoti chake kumutu, n’kukhala ngati waveka bondo lake la
mwendo wamanzere. Ndiyeno anayamba kupukuta thukuta
lomwe linali pachipumi pake ndi dzanja lamanja. Apa mpamene
imvi zake zinaonekera bwino. Pankhope pake panali
pataphulika tsinya lomwe linabwera chifukwa chotopa.
9