Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 11
Matigari
Kenako anayasamula ngati akufuna kumeza munthu.
Sizinali zochita kufunsa kuti anali atatheratu. Chifukwa cha
kutentha, iye ankadzifunsa kuti, “N’chifukwa chiyani dzuwali
likutentha chonchi m’mawa uno ngati wina walituma?”
Posakhalitsa anayamba kuwodzera. Koma maganizo aja
anamubwereranso. Ankadzifunsa kuti, “Ndibwerera bwanji
kunyumba ndekhandekha? Zitheka bwanji kuti ndipite
kunyumba ndili ndekha? Kodi si paja pakhomo pamafunika
kukhala mwamuna, mkazi komanso ana? Tsonotu ndidzuke kuti
ndipite m’milagamu ndikawauze anthu kuti tagonjetsa adani
athu. Ndikasonkhanitse anthu anga, achibale, akazi komanso
ana anga. Tonse tikasonkhane pamodzi n’kubwerera kunyumba
yathu. Kali konkha n’kanyama nthuni. Kodi n’kuiwalilanji
kanyimbo kankakoma kuimba tili ana kaja?
Chikondi ndichoo,
Pakati pa akazi ndi ana.
Timagawana ngakhale nyemba imodzi
Yomwe yagwa pansi panthaka.
Kenako anadzuka n’kuvala chisoti chake chija, kunyamula
chijasi chake ndipo anachiponyanso paphunzi n’kulunjika
kumene maganizo ake anapotokera.
Iye ankafunitsitsa akanapita kaye kukaona nyumba yake,
koma maganizowa akamubwerera, ankadziletsa n’kupitirizabe
kuyenda molunjika m’tauni. Iye anali atatsimikiza mtima.
Ankafuna kuti apite kaye kukafunafuna anthu ake choyamba.
Ankafuna kudziwa kumene anthuwo akukhala, zomwe amadya
ndi kumwa komanso zomwe amavala. Komabe, mtima wake
unkamuthawathawa. Ankafunitsitsa akanapita kukaona
kunyumba kwake, koma ankaonanso kuti sangapiteko yekha.
10