Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 12
Matigari
Mumtima mwake ankati, “Munthu akamayenda ulendo
wapadzikoli amakumanadi ndi misampha komanso mayesero
ambiri.”
Analowa m’munda wina n’kudutsa pakati pa zikanga za
mitengo ya maluwa ndipo kenako anatulukira mumsewu
waphula. Anaima kaye n’kudzayang’ana kumanja, kenako
kumanzere. M’mbali mwa nsewuwo munali magalimoto akuda
a mtundu wa Mercedez-Benz omwe anali ndi mikolamawu.
Kenako anamva mawu kuchokera m’galimoto yomwe inali
kutsogolo kwake. Inali wailesi ndipo inkati:
. . . Mwatsegulayi ndi Wailesi Yanu ya Choonadi . . . Mtsogoleri
wadziko lino, wolemekezeka Pulezidenti Ole, wanena kuti pasapezeke
anthu akuyenda m’magulu a anthu oposa asanu. Iye sanafotokoze
zambiri zomwe zachititsa kuti alamule zimenezi. Koma zikuoneka kuti
ana a kuyunivesite akonza zopanga ziwonetsero panja pa maofesi a
akazembe a dziko la Britain ndi America posonyeza kusagwirizana ndi
zomwe mayikowa akuchita popitirizabe kupereka zida zankhondo
komanso ndalama ku ulamuliro watsankho wa dziko la South Africa . .
. Mtsogoleri wathu Pulezidenti Ole wanena kuti akuyamikira
kwambiri asilikali a dziko la Britain omwe mwezi watha analanda zida
asilikali omwe amafuna kulanda boma. Anati mnzako weniweni
amaoneka pakagwa tsoka. Pulezidenti Ole, wayamikira kwambiri
zimene dziko la Britain linachita polola kuti asilikali ake ena atsale
m’dziko muno kuti aphunzitse asilikali athu kumenya nkhondo.
Pamsonkhano wina, Pulezidenti Ole anabwerezanso zimene ananena
pa nthawi yomwe asilikali a dziko lino ananyanyala ntchito. Iye anati:
“N’zomvetsa chisoni kuti asilikali a boma ananyanyala ntchito kuti
awonjezeredwe malipiro titangolandira kumene ufulu wathu
wodzilamulira. Bwanji sankachita zimenezi pamene tinkalamuliridwa
11