Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 13
Matigari
ndi atsamunda aja? Ndiye zatani kuti ayambe kuchita zimenezi
poyerayera?”
. . . Mukumverayi ndi Wailesi Yanu ya Choonadi. Nduna Yoona
Zachilungamo yanena kuti dziko lathuli ndi la anthu ogwira ntchito.
Ndipo yachenjeza ogwira ntchito onse kuti asiyiretu kugwirizana ndi
anthu omwe akumasokoneza mtendere m’makampani ponena kuti
akufuna awonjezeredwe malipiro. Antchito omwe akumachita zimenezi
sakusiyana ndi asilikali omwe amasokoneza mtendere komanso
kumafuna kulanda boma . . .
Boma lalamula kuti m’dziko muno musapezekenso chipani
chotsutsa . . . Mtsogoleri wa dziko lino, Pulezidenti Ole, wanena kuti
bomali ndi la anthu . . . ndipo anthu m’dziko muno sakufuna kuti
mukhale zipani zotsutsa chifukwa zimabweretsa chisokonezo.
12