Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 14
Matigari
Gawo 4
Anayamba kuyenda m’mbali mwa nsewu n’kudutsa
Mercedes-Benz ija ndipo nkhani zomwe zinkalengezedwa
pawailesi zija zinayamba kumvekera patali.
“. . . Dziko la United States lachenjeza dziko la Russia kuti . . .
Boma la Soviet Union lauza dziko la USA kuti . . . Dziko la China ndi
la India . . . Anthu omwe anapita kumwezi . . . tsopano tifike ku nkhani
zamasewero, mpikisano wamagalimoto . . .”
Iye anadzifunsa kuti, “N’chifukwa chiyani anthu sakuvala
lamba wachilungamo kuti nkhondo komanso zipolowe
zisamachitikenso m’dzikoli?” Mu Benz ija munali anthu awiri
akuda, mwamuna ndi mkazi, ndipo mwamunayo ankatsopa
botolo la mowa wamame, pomwe mkaziyo ankamwa zakumwa
zoziziritsa kukhosi. Kenako anasiya kuganizira zomwe anamva
kuchokera m’galimoto ija, yomwe tsopano inali itapita. M’ma
Benz ena munali azungu okhaokha, ena munali amwenye ndipo
ena munali anthu akuda. M’mbuyomo, bamboyu anali dalaivala
wa Mtsamunda Williams. Koma pano zinthu zinali
zitasinthiratu. Ndi ndani amene akanaganiza kuti tsiku lina
anthu akuda angamadzayendetse magalimoto awoawo!
Chimene chinali chitatsala tsopano chinali choti azipanga okha
magalimoto, sitima zam’madzi, zapamtunda komanso ndege.
Kenako anayambanso kuganizira za banja lake. Ankadzifunsa
kuti, “Ndiyambira pati kuwasakasaka?”
Kenako anatulukira pa ofesi yapolisi yomwe inali m’mbali
mwa nsewu uja. Maganizo enanso anamubwerera. “Kodi
kapena ndikauze apolisi kuti andithandize kuwasakasaka? Ayi.
Ndiwasakasaka ndekha.” Atadutsa polisi ija, anakumana ndi
apolisi awiri ali ndi galu wamkulu. Chapafupi ndi pamene
anakumana nawopa panali chipatala chaching’ono.
13