Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 15
Matigari
Kenako anadutsa apolisi aja n’kumalowera cha kuchikweza
china komwe kunali njanji. Maganizo ake anatembenukirano ku
njanjiyo, yomwe inalowa pakati pa phiri. Zimenezi
zinamukumbutsa zinthu zina moti anakhala ngati wazizidwa.
M’maganizo mwake ankadzifunsa kuti, “Ndi miyoyo ya anthu
angati yomwe inatayika pamene ankamanga njanjiyi komanso
ankaboola phiriri kuti padutse njanji?” Anakumbukiranso
bomba lomwe linaphulika pamalowa komanso mfuu za ogwira
ntchito omwe anakwiririka amoyo bombalo litagwetsa makoma
a phangalo. Anakumbukiranso kubuula koopsa kwa anthu
omwe anaphwanyidwa ndi zitsulo zolemera. Zinkangokhala
ngati akuona zomwe ankaganizazo. Iye ankakhalanso ngati
akumvadi anthu akulira ndi ululu woopsa miyala
itawaphwanya komanso ena akubuula mosonyeza kuti
akutsirizika. Njanjiyo itangotha kumangidwa, inayamba kumeza
masamba atiyi, khofi, thonje, gonje, balele, ndipo tinganene kuti
pafupifupi zokolola zonse zomwe zinkakololedwa panthaka
yomwe Mtsamunda Williams ndi anzake anaba kwa anthu,
zinkatuluka m’dzikoli kudzera panjanjiyi.
Bambo uja anaima pamwamba pa phiri n’kuyang’ana
kumunsi kwake. Tsopano tauni inali itayala konse mpaka
kumunsi kwenikweni kwa phililo. Kumbali zonse kunali mapiri
moti ankangokhala ngati mpanda woteteza tauniyo. Bamboyo
sanamvetse. Ankati kudzayang’ana kutsogolo kwambiri cha
kumapeto a mapiriwo, kenako n’kudzayang’ana tauniyo. Iye
anaonadi kuti yakula zedi poyerekezera ndi kale! Apolisi anali
ndi galu aja anali akumudutsa tsopano. Iye anawayang’ana
mwachidwi pamene ankatsetsereka kulowera nsewu wopita
kumunsi kwa tauniyo.
14