Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 16
Matigari
Kenako anamva kulira kwa sailini kuchokera kufakitale ina.
Sailiniyi inkalira pa 10 koloko ndipo imeneyi inali nthawi
yopumira pang’ono ntchito. Bambo uja anadziyankhulanso
yekha. “Kaya masiku anonso anthu akumapuma mphindi zisanu
zokha basi? Koma amaganiza kuti munthu angapumedi
kanthawi kochepa ngati kameneka? Nthawi imeneyitu ndi
yongokwanira kupita kuchimbudzi kukadzithandiza
mofulumira komanso kukoka chingambwe pang’ono.” Iye
anaganizira za masailini omwe analira nthawi yonse yomwe
anali kutchire kuja. Anaganiziranso za anthu omwe anaduka
manja ndi miyendo komanso ena osawerengeka omwe kwa zaka
zambiri anazunzika kugwira ntchito yakalavulagaga
pafakitaleyi. Anadzifunsa kuti, “Nanga bwanji masiku ano?
Kodi mwina n’kutheka kuti zinthu zinasintha?” Kenako
anakumbukiranso mawu omwe anamva aja. “Boma la anthu . . . ”
Pamene zimenezi zinkayendayenda m’mutu mwake, ankakhala
ngati akuonanso Mercedes-Benz ija, kenako anaganiziranso za
apolisi anakumana nawo ali ndi galu aja komanso chipatala
chija. Kodi zinthu zinalidi zitasintha poyerekeza ndi kale? Iye
anaona kuti apeza yankho la funso limeneli akakafika
kunyumba kwake. Ndipo anatsimikiza mtima kuti sapita kwawo
pokhapokha apeze anthu ake. Iye anadzifunsa kuti, “Kodi
ndiyambira pati kuwasakasaka?” Sailini ija inalilanso ndipo
atangoimva inakhala ngati yamuthandiza kudziwa zochita.
Anadzifunsa kuti, “N’chifukwa chiyani sindinaganize zimenezi
poyamba pompaja?”
Anthu ogwira ntchito pafakitaleyi ankachokera m’madera
onse a m’dzikoli. Kufakitaleko kunkangokhala ngati
kumsonkhano wa ogwira ntchito. Munthu aliyense yemwe
ankafunafuna anthu ake akanayenera kuyambira kumeneko.
15