Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 17
Matigari
Iye anayenda molunjika kumene kunali fakitale ija ndipo
kuti asasochere, ankangotsata utsi wochoka m’chumuni cha
fakitaleyo. Anadutsa ofesi yotumiza makalata, siteshoni ya
sitima komanso malo ena pomwe panali dzimakontena.
Benz anaiona ija inamudutsanso. Kenako anakumananso
ndi apolisi aja. Apolisiwo anali ataima m’mbali mwamsewu
pafupi ndi chipata cholowera m’fakitale ija. Kenako apolisiwo
analowa paziyangoyango penapake ngati akubisalira munthu.
Bambo uja anayenda n’kumalowera komwe kunali chipata
cholowera kufakitaleyo.
16