Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 18
Matigari
Gawo 5
Pachipata cha fakitaleyo panali chikwangwani cholembedwa
ndi mawu akuluakulu kuti:
ANGLO-AMERICAN LEATHER AND PLASTIC WORKS
MALOWA NDI A ENI
Palibe Njira
Fakitaleyo inali yaikulu kwambiri ndipo inazunguliridwa
ndi mpanda wawaya. Fakitaleyo inali mkati mwa mpanda
wamalata ndipo mpanda wakunja unali wawaya
wamingaminga.
Kenako anaona chigalimoto chofiira chikutuluka
m’fakitaleyo. Chinali ndi ngolo zitatu zodzadza ndi zinyalala.
Mlonda anapita kutsogolo kwa chigalimotocho n’kukakweza
chitsulo chomwe chinatchinga pachipatapo ndipo
chigalimotocho chinatuluka. Chitatuluka chinayamba kulowera
kumene kunali chikwangwani china chokembedwa kuti,
“MSIKA WAMASAMBA.” Kenako anayamba kupita kuchipata
kuja.
Mlonda uja anali atakhala pampando. Anavala yunifomu
yakhaki komanso chipewa chofiira chokhala ndi ziyaliyali.
Pajekete yake panalembedwa kuti, “Katundu wa Kampani
Yaulonda.” Pafupi ndi miyendo yake panali kambaula kamakala
kopangidwa ndi chitini. Bambo uja anadzifunsa kuti,
“N’chifukwa chiyani munthu ameneyu akuotha moto kutentha
kumeneku? Mwinatu malungo amupezeketsa?” Kenako
anazindikira kuti mlondayo ankaotcha gunya. Bamboyo anaona
kuti angachite bwino kufunsa mlondayo kuti amuthandize
kupeza abale ake mufakitaleyo. Popeza pafakitaleyi panali
khwimbi la anthu, sankakayikira kuti akhoza kupezapo m’bale
wake. Ankaganizanso kuti mwina mlondayo akhoza kudziwa
17