Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 19
Matigari
komwe kuli ana ake komanso anthu a mtundu wake.
Maganizo akewa anadodometsedwa ndi phokoso la ana ena.
Atatembenuka anaona gulu la ana akuthamanga pakati
pamsewu. Anadzifunsa kuti, “Kodi akuthamangira chiyani?”
Kenako anaona chigalimoto chofiira chija chikutuluka mumsika
muja. Ngolo zake zinali zitadzadza kwambiri ndi zinyalala zina
zomwe inakatenga mumsika muja. Anadzifunsanso kuti,
“Koma nanga n’chifukwa chiyani anawa akuthawa
chigalimotocho? Ana angaaa!”
Sanayankhulenso ndi mlonda uja. Iye anayenda mofulumira
kutsatira ana komanso chigalimoto chija. Mtima wake
unkagunda mofulumira. Iye ankadziuza kuti, “Odi ndifulumire
kuti ndikawauze kuti ndabwera ine bambo awo. Ndikawauze
kuti moyo wothawathawa tsopano watha, ndikufuna
kubwerera kunyumba. Tonse tipite kunyumba kwathu.
Tikalomwe m’nyumba mwathu limodzi. Tikakoleze moto
limodzi. Ndipo pajatu nkhani yomwe inachititsa kuti tilimbane
ndi atsamunda inali yokhudza nyumbayi, si choncho paja?
Tinkafuna nyumba yathu, malo achitetezo, kuti ana athu
azidzasewera pakhonde komanso azidzapanga ndado pabwalo.
Tizidzagawana zochepa zimene tili nazo. Tizidzasangalala
pambuyo pokumana ndi zokhoma, kuzizidwa, kukhaula ndi
njala, kuyenda chinochino chifukwa cha usiwa, kusowa tulo,
kutopa komanso kupulumuka lokumbakumba. Kuti ugonjetse
adani ako umafunika kulimba mtima. Usiku ungatalike bwanji,
kunja kumacha basi.”
Iye sanakhulupirire zimene anaonazi. Anadzifunsa kuti,
“Kodi zimenezi zikuchitikanso masiku ano, m’dziko laufulu
ngati limeneli? Koma zoona zimenezi zikuchitika dzuwa
likuswa mtengo?”
18