Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 20
Matigari
Ana aja anathamanga mokhala ngati akupikisana ndi
chigalimoto chija mpaka anakalowa kumtaya. Malowa anali
aakulu kwambiri ndipo anazunguliridwa ndi mpanda wawaya.
Pampandawo panali pataima akhwangwala ndipo ena anali ali
m’mitengo yomwe inali chapafupi. Nazonso ziwombankhanga
zinkauluka chapatali m’mlengalenga maso awo akuthwa ali
dwii kuyang’ana tianyamata toyendayenda tamiyendo inayi toti
zitole. Gulu la agalu opanda mbuye wawo linalinso balalabalala
pamalowo ndipo ena ankafufuza chakudya pamulu
wazinyalalawo. Azibambo awiri anali ataima pachipata
cholowera kumtayako ndipo zinkaoneka kuti akuuza anawo
kuti akhale pamzere.
“Kodi anawo akuima pamzere kuti atani?” anadzifunsa
choncho. Chigalimoto chija chinalowa kumpanda kuja ndipo
akhwangwala aja anayamba kuitsatira. Nawonso agalu aja
ankathamangira cham’mbalimu, kuilondola kuyembekezera
kuti atole phoso latsikulo. Chigalimotocho chitangokhuthula
zinyalala zija, pamalo onsewo panangoti chifungo guu!
Woyendetsa chigalimotocho anakhuthula zinyalalazo
m’milu itatu. Atangomaliza, agalu, akhwangwala komanso ana
aja anapita pamiluyo n’kuyamba kufukulafukula zinthu.
Apa mpamene anamvetsa chimene chinkachitika. Zikuoneka
kuti mwana aliyense ankayenera kupereka ndalama kuti
alomwe kumtayako. Chimenechi chinali ngati chiphaso
chomuloleza kulowa kumtayako kuti akakanganirane zinthu
ndi agalu, akhwangwala, makoswe, ntchentche komanso
tizilombo tosiyanasiyana todya zowola tomwe tinali pamalowo.
Iwo ankasakasaka ulusi, zigamba, zikopa, zapapati za nsapato,
malabala, zingwe, tomato owola, misonga ya mzimbe, makoko
anthochi, mafupa ndi zina.
19