Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 21
Matigari
Bambo uja anangoima chapatali atachita tsembwe ndi
zimene ankaonazo. Anadandaula kuti, “Ana angaa! Zoona ana
anga?”
Azibambo anaima pachipata aja anachokera limodzi ndi
chigalimoto chija ndipo m’mbuyo mwawo anasiya phokoso la
ana komanso nyama zomwe zinkasakasaka zinthu pamulu wa
zinyalala zija.
“Ndatola wailesi! Ndatola wailesi!” Mnyamata wina
anafuula motero, kwinaku akulumphalumpha, chimwemwe
chitadzadza tsaya.
Posakhalitsa, palibe chinyalala pamulu uja chomwe
chinasiidwa chosatembenuza. Mwana aliyense anali atanyamula
kaphukusi kake ka zinthu. Ena anatola ulusi, makatoni,
mapepala apulasitiki, mapaipi, zigamba zamitundumitundu ndi
chilichonse chomwe anachiona kuti angakachigwiritse ntchito.
Ena anali akutafuna tomato woola, ndipo ena ankatsopa
mokhala ngati akutsukuluza mafupa a nyama omwe anatola.
Kenako anaona ana awiri akukanganirana zingwe za nsapato
ndipo ena anawazungulira n’kumachemerera. Pa ana amene
ankamenyanawo, mwana yemwe ankaoneka wamkuluko
anachipulumutsa chibakera ndipo chinafikira m’mutu mwa
mnzakeyo moti chinamunyamula n’kumugwetsera pansi.
Kenako wamkulu uja anambwandira khosi la mnzakeyo.
Mwana anagwidwa pakhosiyo ankangophiriphitha ngati
nkhuku yomwe ikutsirizika pambuyo poti aionetsa mpeni.
Komabe, mwanayo sanasiye ulusi womwe unali m’manja
mwake uja.
Tsopano bambo uja anatola ndodo n’kuyamba kuthamangira
kunali ana kuja. Mwana ankamenya mnzake uja atangomuona
bamboyo, anamusiya mnzakeyo n’kuthawa ndipo anakaima
20