Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 22
Matigari
chapatali.
Wina uja anadzuka n’kukhala pansi akusisita khosi lake
ndipo anayang’ana bambo uja moyamikira kwambiri. Koma
atangoona kuti bamboyo watenga ndodo, nayenso
anadzambatuka n’kuthawa.
Bambo uja anangoima panja pa mtaya uja. Atakumbukira
kuti tsopano anali atavala lamba wamtendere, anaponyera pansi
ndodo ija ndipo anayamba kutsatira ana aja.
Pamene ankawatsatira, anaona apolisi anali ndi galu aja,
woyendetsa chigalimoto cha zinyalala chija komanso azibambo
ankatolera ndalama kwa ana aja atapanga kamsonkhano kawo
pakatchire kanali pambali pamsewu uja. Anaima moyandikana
kwambiri ndipo pankamveka phokoso la kuwerengera ndalama
zasiliva. Bamboyo anadziyankhulira yekha kuti, “Zoona
anthuwa akugawana ndalama zomwe alandira kuchokera kwa
anawa? Kodi zikuchitikabe kuti anthu ochepa azipindula
chifukwa cha kuzunzika kwa anthu ambiri? Zoona khama
komanso ntchito yakalavulagaga ya anthu ambiri izipindulitsa
anthu ochepa?
Ndi mafunso ngati omwewa omwe anachititsa kuti
azikakhala moyo wothawathawa m’mapiri komanso
kunkhalango kuja. Koma limenelo linali kale. Iye anadzifunsa
kuti, “Nanga n’chifukwa chiyani zinthuzi zikuchitikabe masiku
ano popeza tinalandira ufulu wathu?”
Kenako anakumbukiranso nyumba yake. Iye anali
asanafikeko. Apa njala yokaona kunyumba kwake ija
inamubwereranso ndipo inangokhala ngati yagwirizana ndi
ludzu komanso malikhweru omwe ankalira kumimba kwake
komwe kunakhala pululu kwa masiku ambiri.
21