Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 77
Matigari
Obwera ankhanza inu,
Longedzani katundu wanu muone nsanawanjira!
Popeza eni nyumba,
akubwera kudzalowa m’nyumbayi!
“Atangomva nyimbo imeneyi, mtsamunda uja anathamangi-
ra pamene panali lamya. Ndipo ine ndinathamangira pamene
ankasunga mfuti yake . . . Koma kunena zoona padziko lapansi
pano palibenso chinthu china choipa kwambiri kuposa ukapolo.
Ukapolo ndilibe nawo mawu, ndi kanyama kachabe. Ukapolo
ukaphatikizana ndi umbuli umakhala nsakanizo wachabe.
Umamanga maganizo komanso moyo wamunthu n’kumusiyira
chibaza! Kodi ukuganiza kuti ndi ndani amene anakuwa ku-
chenjeza Mtsamunda Williams? Nanga ukuganiza kuti ndi nda-
ni amene anandilumphira n’kundigwira komanso kunditayitsa
mfuti pamene ndinkafuna kusuntha chala changa kuti ndit-
somphole chopolopolo chikalase Mtsamunda Williams? Uku-
ganiza kuti angakhalenso ndani kuposa John boy!”
“Boy? Wati John Boy? Ukumudziwanso munthu ameneyu?”
munthu wakuda uja anafunsa mosonyeza kuti wadzidzimuka
ndi zimene anamvazo.
“Ndi ndani m’dziko muno amene sadziwa John Boy? Anali
khukhi wa Mtsamunda Williams. Koma munthu amene uja anali
wadyera komanso anali wonenepa zedi. Anali wonenepa ngati
nkhumba. Iyayi, mwinanso ndachepetsa, anali wonenepa ngati
mvuu! Komano munthu angayembekezere zotani kwa munthu
yemwe ankangokhalira kutolera zakudya zotsala patebulo la
Mtsamunda Williams—?”
Thya! Thya!
Matigari anamva ngati thupi lake lang’ambika. Ndipo
76