Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 76
Matigari
“Mwalasa ndithu, ndi yemweyo.”
“Nanenso ndinamvapo za iye. Kodi nawenso ukumudziwa?
Ukudziwa zotani zokhudza mzungu ameneyu?”
“Ndikudziwa zotani zokhudza mzungu ameneyu? Zoona
ineyo ndisadziwe mzungu yemwe ankakolola pamene sanalime
uja? Ndingaiwale bwanji mzungu amene uja, ine munthu
wogwira ntchito, kuiwala mzungu yemwe ankakonda kuchita
masewera a wachiona ndani? Ndiye ukuganiza kuti
chinachititsa kuti tiyambe kulimbana n’chiyani? Chinali chifu-
kwa choti ndinatulukira umambala wake wonse. Ndithu ndina-
bwera komwekuno. Tangoganiza, tsiku lina ndinadzuka,
kusukusula n’kupita kwa Mtsamunda Williams. Ndinamuuza
kuti: ‘Ndinu mtundu wa anthu okhala ngati nthata, mumakhala
pakati pathu n’kumatiyamwanso magazi. Dziwani kuti ngakhale
kunja kutakhala mdima wotani, kunja kumacha basi! Ndipo
masiku onse samacha mofanana. Lero ndi tsiku lina ndipo dzu-
wa likuwala bwino m’mlengalenga. Taleka ndikufunse mafunso
angapo: Kodi ndi ndani amene anamanga nyumba imeneyi?
Ndindani amene anaswa mphanje m’mindayi? Ndiye tsopano
ndimvetsere mosamala. Womanga akufuna umubwezere nyum-
ba yake ndipo wolima akufuna minda yake. Kodi munthu
wokolola pamene sanafese akuganiza kuti iyeyo ndi ndani? Ko-
di akuganiza kuti iyeyo ndiye woimira Mulungu padziko
lapansi pano? Zipita komwe unachokera, chifukwa kuyambira
lero, omanga sakufunanso kuti azichita kupempha malo oti
agone; olima sakufunanso kuti azigona ndi njala; atelala sa-
kufunanso kuyenda osavala; munthu yemwe amagwira ntchito
sakufunanso kusiyira njenjete chuma chomwe amachikhetsera
thukuta. Ndinaimba kuti:
75