Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 78
Matigari
nthawi yomweyo anagwera pansi. Aliyense amene ankaonerera
macheza a anthu awiriwa, sankayembekezera kuti zimenezo zin-
gachitike. Ngakhale Guthera ndi Muriuki anadabwa kwambiri
pamene ankaona nkwapulo ukuuluka m’malere n’kutera
pathupi la Matigari mochita phokoso lalikulu.
Pamene munthu wakudayo ankakwezanso chikwapu chija
kuti amulembe nachonso kachitatu, mzungu uja analowererapo.
“Ugwereni mtima achimwene, chachitika n’chiyani?” anafunsa
adakali pahatchi pomwe paja.
“Eti munthuyu akunyoza bambo anga . . . ine ndikumva. Ndi
wopanda khalidwe! Ofunika kumuphunzitsa mwambo.”
“Wanenanso kuti akuwadziwa? Kodi mesa bambo ako anasowera
limodzi ndi bambo anga?”
“Inde, chitsiruchi chikuoneka kuti chikudziwa zambiri. Ndichium-
budza mpaka chitafotokoza bwinobwino zonse.”
“Mtima pansi. Osaiwala kuti mukungopanga sewero. Mbali yovu-
ta ya seweroli inaseweredwa kale ndi makolo athu. Ukhoza kumufun-
sanso mafunso ena angapo. Mwina angatithandize kudziwa chimene
chinawachitikira.”
Matigari anapititsa manja ake m’chiuno mwake. Koma ana-
kumbukira kuti wadzimanga ndi lamba wamtendere. Monga
munthu wamwamuna, anayesetsa kupirira kuti asaonetsere
pagulu kuti akumva ululu woopsa ndipo anadzuka pamene
anagwera paja mwapang’onopang’ono ngati nkhalamba
yodwala nyamakazi. Kenako anagwira geti lija kuti limuchiri-
kize ngati ndodo yake. Dzuwa linali litabira tsopano, komabe
linasiya kamtambo kofiira ngati magazi komwe kankawalabe
madzulowo. Kamtamboko kankachititsa kuti nyumba ija, pageti
komanso nsewu womwe anthu aja anaima ziziwala.
77