Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 43
Matigari
Gawo 8
Pakhoma pa balayo panajambulidwa chithunzi cha nyama
zakuthengo. Panali njovu, fisi, njati, njoka, kambuku komanso
mbidzi zitakhala mozungulira. Nyama zonsezi zinali
zitanyamula botolo la mowa m’manja mwawo. Mfumu Mkango
ndi imene inakhala pakati pawo, ndipo inkatolera ndalama.
Pachisoti chake chachifumu, panalembedwa kuti “Mfumu ya
M’nkhalango.” Pamimba pake panalembedwa kuti, “msonkho,”
ndipo pafupi ndi miyendo yake panali m’golo wamowa.
Pamgolowo panalembedwa kuti, “Papirani, Papirani. Imwani
Zenizeni! Ndiponsotu Mowa Ndi Wotchipa. ”
Mayi wina wonenepa anakhala pamalo ogulitsira zakumwa
ndipo pamalowa panali potetezedwa ndi zitsulo. Pafupi ndi
mayiyu, panalinso mayi wina wonenepanso ngati yemweyu
ndipo onse anavala madiresi oyera. Azimayiwa ankakambirana
nkhani ya kunyanyala ntchito inali m’kamwam’kamwa ija.
“Ndiye tizitani akatseka fakitaleyi?” Mawu awo ankamvekera
pansipansi chifukwa mtibu wa mubalamo unakwezedwa
kwambiri ndipo pa nthawiyi n’kuti pakuseweredwa nyimbo
yakuti “Shauri Yako*.”
*Shauri Yako (Kiswahili): Kutanthuza: kuti “Limenelo ndi vuto lako, zako zimenezo.”
Matigari ndi Muriuki anakhala patebulo lapakona
chakumapeto kwanikweni kwa balayo. Matigari anakoleka
chipewa komanso chijasi chake chija pampando.
Mayi mmodzi anatuluka kogulitsira kunja n’kudzawafunsa
kuti akonda kudya chiyani.
“Kodi masiku ano azimayi amagwiranso ntchito kubala?”
Matigari anafunsa Muriuki.
“Azimayitu amagwira ntchito paliponse,” anayankha motero
42