Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 44
Matigari
Muriuki. “Amasesa kufakitale, amapalira m’minda, amathyola
tiyi ndi khofi, amafukula mapaipi otsekeka komanso amakonza
ngalande zodutsa madzi onunkha.”
“Nanga mayi ako? Mayi ako amagwira ntchito yanji?”
“Mayi anga? Mayi angatu anamwalira.”
“Ulibe bambo komanso mayi? Ndiye kuti ndiwe mwana
wamasiye? Chinawachitikira n’chiyani mayi akowo?
Ankadwala?”
“Munthu wina anayatsa nyumba yathu ndipo mayi anga
anapsera momwemo.”
“Munthu wina anayatsa nyumba? Anayatsayo ndi ndani?”
“Alandilodi athu. Mayi anga ankapanga lendi nyumba ya
munthu wina koma ankalephera kulipira. Ndiye tsiku lina
alandilodi anawauza kuti atulukemo m’nyumbamo, koma mayi
anga anakana. Anawauza kuti: ‘Mukuganiza kuti ndilowera kuti
mukandithamangitsa m’nyumbayi? Simunganditulutse
m’nyumbamu n’kundisiya patchire ngati nyama. Zoona mulibe
chisoni! Mukufuna kuti ndife? Kodi ndalama ndi moyo wa
munthu chofunika kwambiri n’chiyani?’ Ndiyendo alandilodiwo
anati: ‘Mutuluke m’nyumba yangayi! Muona kolowera, ine
ndiye ndizikakudyerani kuchipatala? Mutulukemo
m’nyumbamu kaya mukufuna kapena ayi. Muchoke pano tatopa
nanu!’ Madzulo a tsikulo, mayi anabwera kunyumba ataledzera
ndipo anangofikira kugona. Chapakati pa usiku,
ndinadzidzimuka nditamva fungo la utsi. Ndinathamangira
kumene amayi anagona koma ndinawapeza atatapatikiratu ndi
tulo. Ndinayesetsa kuwagunyuza, ndipo anadzukadi.
Ananditulutsa panja kudzera pazenera. Koma iwowo
sanakwanepo chifukwa zeneralo linali laling’ono. Ndiyeno
43