Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | 页面 42

Matigari ankathamangira kuntchito zawo zomwe zinkayamba 2 koloko. Kenako panadutsa apolisi awiri ali ndi galu m’manja ndipo ankalowera chakumene kunali mashopu kuja. Kunja kunkatentha kwambiri. Matigari ndi Muriuki analowa m’malo ogulitsira zakudya muja n’kudutsa mpaka kukalowa m’kati mwa bala ija. Kenako kunamveka phokoso la kulira kwa sairini. Nthawi tsopano inali itakwana 2 koloko. 41