Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 30
Matigari
padzakhala mtendere ngati kumwamba.
N’kutheka kuti sanamve pamene mwana uja
ankamuchenjeza kuti asalowe m’mudziwo. Iye anayendabe
ngati njovu kulowa m’mudzi wa ana uja.
Kenako anangozindikira mwala wamudutsa. Mwamwayi
unamuphonya chifukwa ukanamupeza ukanamuchotsa diso.
Posakhalitsa winanso unatera pafupi ndi mwendo wake.
Anangozindikira winanso ukubwera ngati wapalegeni moti
akanapanda kuzinda ukanamuswa. Apa mpamene anazindikira
kuti anawo amagenda iyeyo. Mwana ankamenya mnzake uja
anali ataima pamwamba pa Mercedes-Benz, akuitana anzake
n’kumawauza kuti m’mudzi mwawo mwalowa m’maliwongo
yemwe akufuna kuwabera zinthu zimene atola.
Kenako bambo uja anaima kwi!
Pa nthawiyi n’kuti miyala ija ikuvumbwa kuchokera mbali
zonse. Kenako anapalapasa m’chiuno mwake pamene ankaika
pistole yake ija, koma anakumbukira kuti wavala lamba
wamtendere. Komanso anazindikira kuti anali ana chabe, sanali
ngati mdani analimbana naye kwa zilumika zambirimbiri uja.
Modabwa ndi zimene zinkachitikazo, anaima njo n’kunena kuti,
“Ana anga!”
Mwana anali naye uja anazindikira kuti paipa.
Anathamanga n’kukamugwira bamboyo mkono n’kuyamba
kutuluka naye m’mudzi muja.
Bamboyo anayamba kutsatira mwanayo asakumvetsa kuti
chikuchitika n’chiyani. Ana ena aja ataona kuti akuthawa,
anayamba kukuwa kwinaku akuvunga miyala mwamphamvu
n’kumamuperekeza nayo bamboyo pamene ankathawa
molowera kumene kunali chipata cha fakitale ija. Pa nthawiyi
n’kuti nkhope yake itagwa chifukwa cha chisoni ndi zimene
29