Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 29
Matigari
onse.
Bamboyo anadzifunsa kuti, “Zomwe zinkachitika kale zija si
izi zikuchitikanso lerozi? Zinkachitika kale, zikuchitikanso
masiku ano. Kodi tidzasiya liti kuona malodza amenewa?”
Mtima wake unapopa magazi mwamphamvu ndipo
zinkangokhala ngati nawonso ubongo wake ukuchita zomwezo.
Iye ankangolakalaka atakumbatira ana onse n’kuwatenga kupita
nawo kunyumba yake nthawi yomweyo. Iye ankafuna kutenga
anawa n’kupita nawo kunyumba ija yomwe iye ndi Mtsamunda
Williams anakhala akumenyanirana zaka zapitazo. Nyumba
yomwe inachititsa kuti azikhala moyo wothawathawa m’mapiri
komanso m’nkhalango. Anadzifunsa kuti, “Kodi panja
tinkaimba nyimbo iti?
Timagawana ngakhale nyemba imodzi,
yomwe yagwa pansi panthaka.
Nyemba imodzi yomwe tinaivutikira . . . ”
Iye ankadziona akulowa nyumba yake ija limodzi ndi ana
ake, akuyatsa moto komanso akugwira ntchito zapakhomo
limodzi, utsi ukutuluka m’chumuni cha nyumba yawo. Iye
anatsimikiza mtima kuti anawo adzachoka kumanda a galimoto
ankakhalawo komwe ankakhala moyo wozunzika kwambiri. Iye
ankaona kuti anawo ayenera kuyambanso kukhala moyo
wabwino, osati womangodyeredwa masuku pamutu. Ankafuna
kuti anawo akakhale m’nyumba yatsopano. Malo abwino ngati
paradaiso. Koma kenako m’mutu mwake munabwera maganizo
ena. “Zimenezitu zitheka! Palibe chimene chingalake anthu
amanja omwe akuchita zinthu mogwirizana.” Pamene
ankaganiza zimenezi, anangopezeka kuti akuyenda kulowera
kunali ziphapha zagalimoto zija kuti akawauze anawo zimene
ankaganizazi. Kuti zinthu zidzasintha ndipo padzikoli
28