Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 28
Matigari
“Anafa akumenyera ufulu . . . ” bamboyo anatero, akuoneka
kuti maganizo ake ali kutali. “Omenyera ufulu wa dziko lathu,
mafakitale athu komanso nyumba zathu.”
“Ali kuti?” mwanayo anafunsa akuoneka kuti akufunadi
kudziwa yankho la funso lakeli.
“Komadi, kaya ali kuti?” bamboyo anabwereza funsolo ngati
kuti nayenso akusinkhasinkha yankho lake. Koma mwana uja
anamudulira kutsogolo n’kumuuza kuti:
“Basi, mukhoza kubwerera pano. Nyumba zathu zija ndi
zimenezi.”
Pa nthawiyi n’kuti atangodutsa nyumba zina zosanjikizana.
Kutsogolo kwawo kunali manda a galimoto zosiyanasiyana.
Ziphapha za galimoto monga Ford, Mercedes-Benz,
Volkswagen, Peugeot, Volvo, Fiat, Datsun ndi zina, zinali nduu
pamalowo. Analidi manda enieni a ziphapha za galimoto. Ena
anali opindikapindika, ena ophwanyikiratu moti anangotsala
zitsulo zokha, kungosiya mbiri yoti nthawi inayake inali
galimoto. Malowa kunalidi kunsitu kwa galimoto
zosiyanasiyana.
Ziphapha zokutha kwambiri zinali zitaphimbidwa ndi
makatoni, mapepala apulasitiki, masaka, nsalu komanso zinthu
zolekanalekana. Zina zinali zitakhazikidwa pamiyala pomwe
zina, mkati mwake munkamera udzu.
“Zimenezi ndiye nyumba zathu!” anatero mwana uja.
“Izizi?”
“Inde, umenewu ndiye mudzi wathu. Aliyense wa ife ali ndi
nyumba yake. Nyumba yanga ndi Mercedes-Benz,” mwanayo
ananena zimenezi monyadira kwambiri mokhala ngati akuuza
bamboyo kuti nyumba yakeyo ndi yapamwamba kuposa za ena
27