Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 27
Matigari
“Ayi, ndinawasiya ndi ineyo. Choyamba ndinalandidwa
nyumba yanga, kenako ana anga anabalalikira mbali
zosiyanasiyana za dziko lino.”
“Zinachitika liti zimenezo?”
“Ii! Kalekale, kale kwambiri.”
“Ndiye munali kuti zaka zonsezi? N’chifukwa chiyani
simunaganize zowafunafuna zaka zapitazo?”
Bamboyo anamezera mate. Ankasinkhasinkha kuti amuuza
bwanji mwanayo kuti wakhala akulimbana ndi atsamunda kuti
amubwezere nyumba yake! Ankaganizira kuti amufotokozera
bwanji kuti kwa zaka zosawerengeka wakhala akulimbanana
ndi Mtsamunda Williams n’cholinga choti ana ake asazunzike.
Kenako anaganiza zouza m’nyamatayo mavuto omwe
anakumana nawo pamoyo wake pamene ankalimbana ndi
Mtsamunda Williams n’kumakhala moyo wothawathawa
m’nkhalango, kumabisala m’mapiri, m’zigwa, m’mapanga,
mitsinje komanso malo ena osiyanasiyana.
“Ndinayamba kuwasakasaka zaka zapitazo.” Bamboyo
anaitumbula motero nkhaniyo, koma pamene ankati
adziiphinya, Muriuki anasintha nkhani.
“Koma mungawazindikire mutakumana nawo?”
“Amaoneka ngati iweyo, komanso anthu ena onse. Moti
iweyo ukungooneka ngati unabadwa bere limodzi ndi ana anga.
Zikungokhala ngati munabadwa kwa mayi m’modzi, bambo
m’modzi.”
“Inetu bambo anga anamwalira,” anatero mwanayo.
“Ndinamva zoti anaphedwa pamene ankamenyera ufulu wa
dziko lino.”
26