Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 26
Matigari
“Inde.”
“Tiyeni ndikakuonetseni.”
Anayenda n’kudutsa msika uja n’kutenga njira yolowera
kumanzere ndipo anatulukira pashopu ina yaikulu yomwe inali
m’nyumba yansanjika. Nyumbayi inali chakumanja kwawo.
Anayenda n’kudutsa banki ya Barclays, kampani ya insulansi ya
American Life komanso kampani ya fodya ya British-American
Tobacco. Kenako anadutsa pafupi ndi malo omwetsera mafuta a
galimoto.
“N’chifukwa chiyani pamalowa paunjikana magalimoto
onsewa?” bambo uja anafunsa mwana uja.
“Mukunena magalimoto awawa? Ingoisiyani nkhani
imeneyo. Mukamadzadutsanso pamalo ano tsiku lina
mudzadabwa. Nthawi zina malo amenewa amadzadza mabezi
okhaokha. Mukhoza kudzaganiza kuti mabenziwo
amapangidwa pomwepa. Eni a mabenzi amenewo amapita
kukachita nacho chakumwa kuhotelo iyo, hotelo ya New
Sheraton.”
Zimene mwanayu ankanena zinali zoonadi, chapoteropo
kunkaoneka chinyumba chansanjika zinayi chomwe chinali
pakati pa mitengo ya paini, ndipo pabwalo pake panali mitundu
yosiyanasiyana ya maluwa omasura bwino.
“Pamene ndinkachoka kuno, apapa panalibepo kanthu,”
bamboyo anatero.
Kodi inuyo mukufuna chiyani?” mwana uja anafunsa
bamboyo. Pa nthawiyi n’kuti ana ena aja atazimiririka.
“Ndikufunafuna ana anga.”
“Ana anu? Ana anuwo anathawa kunyumba n’kubwera
m’tauni muno?”
25