Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 25
Matigari
“Azibambo enaake, anthu ngati inuyo,” mwanayo
anayankha motero. Kenako anamezera mate n’kunena kuti,
“Koma akayerekezanso kuchita zimenezi aona mbwadza.”
“Bwanji?”
“Taphunzira njira zodzitetezera. Tikumawagenda ndi
miyala, apo ayi tikumagwira m’modzi ndikumuphwanya.”
“N’chifukwa chiyani mumalipira kuti mulowe kumtaya
kuja? Kodi mumakhala mukulipira msonkho kapena?”
“Ayi. Azibambo awiri munawaona aja anangoyamba
kumaima pageti paja n’kumatiuza kuti tiziwalipira.”
“Chimachitika n’chiyani ngati simunalipire?”
“Ee! Amatikhudula! Tsiku lina anatiwaza mambama.”
“N’chifukwa chiyani simunangogwirizana kuti muwatibule
kapena kuwagenda ngati mmene wanenera muja? Mwinanso
munakangopita kupolisi n’kukawanenera.”
“Kupolisi? Mulitu ndi chibwana inu! Apolisi ake ati? Poti
apolisi ndi mbava zimenezi amadziwana. Anthu amenewa
amangoti khethekhethe ngati zala za dzanja langali,” anatero
mwana uja akumusonyeza bambo uja dzanja lake.
“Tikangopanda kupereka, apolisi amayamba kutisakasaka
n’kumanena kuti taba zinthu, kapena kutiletsa kulowa
kumtaya kuja ponena kuti tikatengako kolera n’kupatsira anthu
ena. Nthawi zina amatithamangitsa m’nyumba zathu
n’kumanena kuti ndife amasikini.”
“Umakhala kuti?”
“Kunyumba yanga.”
“Nyumba yako? Ili kuti?”
“Mukufuna mukaione?”
24