Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 24
Matigari
Gawo 6
Mwana ankamenyedwa uja ankaopabe mnzake
anamumenya uja. Iye ankayenda pang’onopang’ono
chakumbuyo kwenikweni kwa gulu la anzakewo. Kenako
bambo uja anamupeza. Mwanayo sanazindikire kuti bamboyo
akubwera m’mbuyo mwake mpaka pamene anamupeza.
Atangozindikira kuti pambali pake pali munthu,
anadzidzimuka.
“Usaope, ndataya ndodo ija.” Bamboyo anatero.
Bamboyo ndi mwanayo anayenda kwa kanthawi
asakuyankhulana. Zovala za mwanayo zinali zigamba
zokhazokha ndipo nsapato yomwe anavala inkamwetulira moti
zala zake zinkaonekera zikusuzumira.
“N’chifukwa chiyani mukutilondola?” mwanayo anafunsa
bamboyo motero. “Kodi nanunso mukufuna kutibera zinthu
zimene tatolazi? Komatu zinthu zimenezi ndi zathu, ndipo ndi
phindu limene tapeza, mukudziwa?”
“Phindu?” bamboyo anafunsa motero posamvetsa kuti
mwanayo akutanthauza chiyani.
“Inde, limeneli ndi phindu limene timapeza, zinthu zomwe
timatola kumtaya kuja,” mwanayo anatero akumuonetsa zingwe
zomwe mnzake uja ankafuna kumulanda.
“Kodi anthu ena amakuberaninso zimene mumatolazi?”
“Inde amatibera! Akaona kuti tatola zinthu zabwino monga
nsapato, malamba komanso zikopa, amabwera akutikukutira
mano n’kumatiuza kuti: ‘Kodi zinthu zimenezi mwazitenga kuti,
ana akuba inu?’”
“Ndi ndani amachita zimenezowo?”
23