Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 31
Matigari
zinkachitikazo.
Tsinya linali pholipholi pachipumi. Zinkaoneka kuti anali
ndi mwayi kwambiri chifukwa miyalayo inkangomuphonya.
Palibe mwala womwe unamufika m’nthupi.
Galimoto zonyamula mabwana a ku Ulaya, ku Asia
komanso ku Africa zinkangoti vuu, vuu! Ena anaimitsa galimoto
zawo kuti apereke mpata kwa oyenda pansi kuti awoloke
kwinaku akusangalala kuonerera gulu la ana lija litapanikiza
munthu wachikulire ndi miyala. Ena ankangoonerera ali
m’magalimoto awo sewero lomwe linkachitikalo. Ena anali
atatsamira galimoto zawo, kwinaku akupyontha Co ca-cola ndipo
ena ndudu zinali zili pakamwa, utsi uli phaa! Panalinso ena
ambiri omwe ankaonerera zimene zinkachitikazi. Eniake a
maokala komanso ogula malonda anaima m’makomo komanso
panja ali m’magulu n’kumaonerera munthu wamkulu
atapezeketsedwa ndi miyala.
“N’chifukwa chiyani anawa akugenda wamisalayo?” ena
anafunsa. Ena ankangopukusa mitu n’kunena kuti, “Ana ndi
amisala amadana kwambiri. Amangokhala ngati mphaka ndi
khoswe.”
Bambo uja sanasinthe mmene ankayendera komanso
ankaoneka kuti sakuzindikira kuti ali pangozi yaikulu.
Anachotsa chijasi chake chija kuchoka paphunzi lina n’kuchiika
paphuzi lina. Pamenepo n’kuti pachipata cholowera kufakitale
kuja pakutuluka unyinji wa ogwira ntchito omwe ankapita
kukadya nkhomaliro. Mwana uja anamusiya bambo uja
n’kuthawira kuchipata kuja. Bamboyo anatsala yekha pakatikati
pa anthu oonerera, ogwira ntchito kufakitale aja komanso ana
ankamugenda aja. Pa nthawiyo kunja kunkatentha ngati
muuvuni.
30