Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 3
Matigari
mwini nyumbayo n’kukhala pakhonde, alendowa anatenga ma-
lo onse abwinoabwino.
Anatenganso chilichonse chaphindu kuphatikizapo
mphamvu za eni malowo. N’kupita kwa nthawi chifukwa cha
kulimba mtima kwa anthu omenyera ufulu wadziko lawo,
anakakamizika kupereka ufulu, koma anapitirizabe kulamulira
pogwiritsa ntchito anthu ena akuda omwe anawaika pamipando
ndipo nawonso anayamba kupondereza anzawo aja ndi nkhan-
za zosaneneka.
Buku la Matigari limasonyeza nkhondo zomwe zinachitika
pakati pa anthu omenyera ufulu wawo ndi olamulira achit-
samunda omwe ankafuna kumanga maganizo a anthu akuda
mu ukapolo. Koma ena ozindikira komanso olimba mtima anai-
ma nazo n’kuyamba kunena kuti zinthu zomwe anazikhetsera
thukuta zibwerere kwa eni ake. Anthuwa anayamba kukana kuti
atsamunda komanso antchito awo azikolola pamene sanalime.
Limasonyezanso zimene boma linkachita kuti m’malo mothan-
diza anthu linkakonda kuchita zinthu zoti mayiko ena alitame.
Komabe sindigwirizana kwenikweni ndi zimene Ngugi ana-
sonyeza m’bukuli kuti choonadi ndi chilungamo chingapezeke
kokha ngati anthu atagwiritsa ntchito mphamvu polimbana ndi
amene akuwaponderezawo, mwinanso kufika pokhala okonze-
ka kufa pomenyera ufulu wawo. Ine ndimaona kuti zimenezi
zimangokolezera mavuto. Mfundo yosatsutsika imene
ndimaona ndi yoti anthu sangakwanitse kulamulirana okhaokha
zinthu n’kumayenda popanda vuto lililonse. Chifukwa cha ku-
chuluka kwa anthu adyera m’dzikoli, anthu ambiri
amapwetekeka chifukwa cha zochita za anthu ochepa odzikon-
da. Ngugi anapereka chithunzi chabwino cha zimene zimachi-
tika anthu akakhala ndi mtima wa kokerakwako.
2