Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 2
Matigari
Mawu Oyamba
Buku la Matigari linalembedwa ndi Ngugi wa Thiong’o
ndipo linasindikizidwa koyamba ndi kampani ya Heinmann
mu 1989. Bukuli linamasuliridwa m’Chichewa chothyakuka ndi
Bonwell Rodgers. Mwachidule, bukuli limafotokokoza za
msilikali wina wagulu la Mau Mau yemwe anabwerera kwawo
atakwirira zida zake n’kuvala “lamba wamtendere.” Iye ankafu-
nitsitsa kukasonkhanitsanso anthu a mtundu wake komanso
kuyamba moyo watsopano. Koma m’malo mwake anakapeza
dziko litazondoka, zinthu zisakuyenda mmene ankaganizira.
Kuti akonze zinthu, anayamba kufunafuna choonadi ndi chi-
lungamo. Iye anazungulira m’dziko lonse koma sanapeze pame-
ne pankachitika chilungamo ndipo anapeza kuti anthu ake
ankangolimidwa pamsana ndi atsogoleri achinyengo omwe
ankangofuna kukhutitsa mimba zawo. Pamapeto pake anapeza
kuti ntchito yake yofunafuna choonadi ndi chilungamo
inangopita padera.
M’bukuli Ngugi anasonyeza kuti anthu akhoza kupitirizabe
kuponderezedwa ndi olamulira awo ngati patapanda kupezeka
munthu wolimba mtima woti ayankhule komanso amenye
nkhondo n’kuthetsa kupanda chilungamoko.
Bukuli limafutukula mmene atsamunda anakokotera chuma
cha ku Africa kuno n’kuwasiya eni dziko akuzunzika koopsa ndi
umphawi. Limasonyeza kuti alendowa anabwera kudzapempha
malo, koma ankasangalala kuposa eni dziko. Kenako anayamba
kulanda malo ndi zinthu zina moti anasiya eni malowo manja ali
m’khosi. Mofanana ndi njovu yomwe inapempha muthu wina
malo oti ibisale mvula, n’kupezeka kuti yadzadza m’nyumbamo
1