Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 267

Matigari Gawo 20 "Munathawa bwanji?" Guthera anafunsa Matigari. "Ndinathawa kudzera pawindo!" Matigari anayankha mtima wake ukumupweteka kwambiri. Koma iye anayang'ana chakutsogolo mokhala ngati akuyang'ana winawake chapatali. "Kodi simumaopa, simumaopa pamene anakulozetsani mifuti paja?" Muriuki anafunsa. "Ndi ndani amene sangachite mantha zitamuchitikira zim- enezo?" Matigari anayankha. "Koma timangofunika kuphunzira kulimbana ndi mantha. Tifunika kumenya nkhondo yolimbana ndi mantha amene alowa m'dziko lathuli. Mantha ndi mdani wa anthu. Amachititsa kuti m'dziko mukhale mavuto ambiri . . . Ko- ma kodi munakwanitsa bwanji kudziwa komwe ndinali?" "Chipewa chanu," Guthera anatero. "Chinagwera kuti?" Muriuki anafunsa. "Sindikudziwa pamene chinagwera," Matigari anayankha, "Koma musadandaule, chakwaniritsa cholinga chake. Chakuthandizani kuti mudziwe kumene ndili." "Inetu ndimaganiza kuti mwapsera m'nyumba momwe mu- ja," anatero Guthera. "Ine ndimaganiza kuti akumangani basi," Muriuki anatero. "Mwinanso kukuwomberani!" Guthera anawonjezera. Matigari, Guthera ndi Muriuki anali akupuma paphiri lina. Kunja kunali kuli m'dima, koma Matigari ankadziwa njira zonse. Iwo anayamba kuyenda molowera kumene kunali mtengo wakachere kuja, komwe Matigari anabisa zida zake: AK47, pistole, lamba wazipolopolo komanso chikandalanga. Chapatali kwambiri ankatha kuonabe kuwala kwa moto womwe 266