Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 266

Matigari Pamenepo ndiye panayambika chintchito chofufuza. Iwo anatembenuza zitini zonse kufunafuna Matigari. Ntchito yofufu- zayi inayamika moto uja udakalilima panyumba ija. Koma apoli- si komanso asilikali ankafufuzawa ankadzifunsa kuti: ‘Kodi Matigari ndi ndani?’ Enanso ankafunsana okhaokha. “Kodi timuzindikira bwanji popeza sitinamuonepo? Kodi amaoneka bwanji? Kodi ndi mtundu wanji wa munthu? Kodi ndi mzimayi kapena mzibambo? Kodi ndi mwana kapena munthu wamkulu? Kodi ndi wonenepa kapena woonda? Kodi ndi weniweni kapena wongopeka? Kodi Matigari ma Njiruungi ndi ndani kwenikweni? Kodi ndi munthu kapena mzimu?” 265