Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 265

Matigari ambiri ankati: ‘Ayenera kuti anachita kulinganiza bwino chi- wembuchi.’ Nkhaniyi itafika kwa Pulezidenti Ole, nthawi yomweyo ana- lengeza lamulo latsopano, ‘Womberani onse omwe akusokoneza, iphani aliyense wosokoneza.’ Kenako ananena kuti, ‘Matigari ayenera kupititsidwa kunyumba ya boma wam o yo k apena wakufa.’ Asilikali ena anatsala pamalo aja n’kumadikirira kuti moto uja uzime n’cholinga choti ukazima ayambe kuyang’anayan- g’ana thupi la Matigari. Iwo ankaganiza kuti wapsera m’nyumba muja. Ozimitsa moto atafika, ankasowa poyambira kulimbana ndi motowo chifukwa unali waukulu zedi. Onse anangoimaima pan- ja paja n’kumangozungulirazungulira, ndipo masailini analira mpaka pakati pausiku. Asilikali ena ambiri anayamba kufika m’malole. Iwo anatha- manga kuti akateteze nyumba zomwe zinali zisanayatsidwe kapena kuphwanyidwa ndi anthu olusa aja. Ndi Guceru amene anazindikira chipewa cha Matigari chili pansi pafupi ndi geti lolowera kunyumba ija. Wotsogolera apolisi uja anaitanitsa agalu . . . Kenako apolisi awiri ali ndi agalu akuluakulu ngati mikango anafika. Agalu aja anayamba kununkhiza fungo. “Mubweretse Matigari, wamoyo kapena wakufa,” wot- sogolera uja analamula, potsatira zimene Pulezidenti Ole analamula. Iye analonjeza apolisi komanso asilikaliwo kuti ame- ne abweretse Matigari alandira mapaundi 5,000. 264