Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 268
Matigari
unkaulukira m'mwamba.
"Kunja kumachita mdima waukulu kwambiri kukatsala
pang'ono kucha," Guthera anatero.
"Inde, kwatsaladi pang'ono kucha," Matigari anayankha.
"Mwandikumbutsa nyimbo ina yomwe tinkakonda kuimba.
Kunjaku kukanachaa,
Kunjaku kukanachaa,
n'kadapita kukasamba madzi ozizira limodzi ndi mbalame zam'mawa
Kunja kwacha tsopano, ndipo dzuwa lawala.
Asanamalize kuimba nyimboyo, anamva kulira kwa agalu.
"Anthu ena akutitsatira," anatero Matigari. "Koma musaope,
konzekani, chifukwa chimenechi ndi chiyambi chabe
chamikwingwirima imene tikumane nayo."
"Kodi agaluwo akulira kuchokera kuti?" Muriuki anafunsa.
"Ali m'chigwa chomwe tadutsa chija," Matigari anatero.
Kenako anatsetsereka kuchokera paphiri paja
mwakachetechete. M'mbuyo mwawo ankatha kuona matochi a
apolisi omwe ankawatsatawo. Matochiwo
ankangoyandikirayandikirabe, ndipo posakhalitsa
anawayandikira kwambiri.
"Ngati titafulumira kwambiri tikhoza kukafika kumene kuli
mtengo wamkuyu ndakhala ndikukuuzani uja apolisiwo
asanatipeze." anatero Matigari, powalimbikitsa.
"Ndikakangovala lamba wanga, palibe wapolisi amene
angayerekeze kukawoloka mtsinje, olo atakakhala zikwizikwi."
Apolisi aja anawasakasaka usiku wonse. Kenako kunja
kunayamba kuwala. Matigari, Guthera ndi Muriuki anali
atatheratu. Mtsinje uja sunali kutali, koma kulira kwa agalu
267