Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 258

Matigari Iwo anazindikira kuti apolisi akumutsata ndipo chidwi chawo chinali pagalimoto za apolisi zomwe zinkayenda pang'onopang'ono m'mbuyo mwa Matigari zija. Iwo sankadziwa kuti chamuchitikira n'chiyani kuti azilondoledwa ndi apolisiwo komanso kuti akanatani kuti adzipulumutse. Iye anali atazungu- liridwa ndi adani. Apolisi omwe anaima pageti lolowera kumpanda wanyumba ija anatsegula geti ndipo anachita saluti n'kulola kuti Matigari alowe kumpandako. Iwo sankadziwa kuti akulowetsa chilombo. Ankangodzifunsa kuti: ‘Kodi nduna imene yabwerayi ndiye iti?’ Aliyense ankadzifunsa funso lomweli. ‘Kodi kumbuyo kwa Mer- cedes-Benz'yo kunali nduna iti?’ Komabe sankadabwa kwenikweni ndi kubwera kwa ndunayo kuchochitikachi. Iwo ankadziwa bwino mmene m'mimba kwa akuluakulu a boma ko- manso achipani cholamula munkabwadamukira akaganizira za kubweranso kwa Matigari ma Njiruungi. Iwo ankaganiza kuti, ‘Ngakhale Matigari atakhala kuti ndi Khristu, ayenera kuman- gidwa mwansanga kapena kuwomberedwa akabwera ku- malowa.’ Matigari anayendetsa galimoto ija n'kumalowera chakugala- ja, ndipo mofulumira anaponda buleki ndipo galimotoyo ina- khwekhwereka n’kutembenuka, moti mphuno yake inaloza ku- mene kunali geti kuja. Kenako anaiyendetsa mpaka pamene panali khomo lolowera m'nyumba ija. Galimoto za apolisi zinkayenda pang'onopang'ono zija zinai- ma mwadzidzidzi panja paja. Apolisi omwe anali m'galimotozo anatuluka mofulumira mifuti ili m'manja. Giceru, kazitape uja anatulukanso nawo limodzi. Wina ananyamula kawailesi meseji m'manja ndipo anayamba kuyankhula. 257