Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 257

Matigari pa nyumbayi anali ngwee, ndipo panja pake pankawala bwinob- wino kuchokera mbali zonse zozungulira nyumbayo. Magetsiwo ankaunikanso nkhope za anthu omwe anaima pafupi ndi nyumbayi. Apolisi ena ankayendayenda pamalowa atagwira agalu. Ulendo uno sanali apolisi awiri okha aja omwe Matigari ana- kumana nawo, koma anali ambirimbiri. Zinkangokhala ngati na- wonso agaluwo anabwera kudzaona Matigari ma Njiruungi. Fumbi la anthu lija litangoona galimoto ya mtundu wa Mer- cedes-Benz, pambuyo likutsatiridwa ndi galimoto ziwiri za apolisi, linaganiza kuti ndi nduna kapena munthu wina wole- mekezeka kwambiri wa m'boma. Iwo anaganiza kuti, Matigari ayeneradi ndi patali ndithu. Iwo ankaona kuti anthu ambiri amamuopa ataona munthu wolemekezeka wa m'boma akubwera kudzamuona akubweran- so kachiwiri, anthuwo anaganiza choncho. Apolisi omwe ankamutsatira m'mbuyo aja anasangalala kwambiri ataona kuti Matigari alibenso kolowera. Iwo ankadzi- uza kuti, "Aha! tamukamata tsopano." Iwo ankadziwa kuti nsewu anatengawo sunkapita patali ndipo iwo anayamba ku- chepetsa liwiro molimba mtima. Palibe ngakhale m'modzi wa anthu amene anabwera pa- malowo amene anazindikira chimene chinkachitika. Ndi Guthera ndi Muriuki okha amene anadziwa zimenezi. Komabe iwo sankadziwa kuti Matigari abwera motani ku- malowa. ‘Kodi timudziwitsa bwanji kuti abwere kumene tili kuno?’ ankadzifunsa ali pakati pa ana aja. Mitima yawo inanyamuka ataona Matigari ali pachiwongole- ro m'galimoto ya Mercedes-Benz ija. 256