Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 259

Matigari Anthu anali panja panyumba aja anangozindikira apolisi ko- manso asilikali aja akukhamukira kunyumba ija n’kuizungulira. Kenako kunatulukira malole odzadza ndi asilikali, ndipo mifuti yawo inali yotcheratchera. Apa ndi pamene anthu aja anaitolera. Anazindikira kuti m'galimoto muja munali Matigari. Iwo anayamba kukuwa kuti, "Matigari ma Njiruungi! Matigari ma Njiruungi!" Kenako wapolisi yemwe ankatsogolera anzake anaima pam- wamba pa Land-Lover ndipo anayamba kuyankhula ndi khwimbi la anthu lija kudzera pachimkuzamawu. "M'nyumbamu mwalowa zigawenga zoopsa kwambiri." iye anatero. "Ndipo zili ndi zida zoopsa!" Kenako anatembenukira kunyumba ija n'kuperekanso chilengezo china. Wapolisiyu anali ndi mawu amphamvu kwambiri ndipo ankamveka ponseponse mumdima wangati im- fa womwe unali usikuwo. "Iwe Matigari komanso omwe akukutsatirawo, kaya anza- kowo ndi ndani, mukuyenera kuimika manja! Mwazungulirid- wa mbali zonse ndi apolisi komanso asilikali. Ingo im ik ani m anja basi! Tulukani m' nyumbamo, mutaimika manja m' mwamba. Mukachi- ta zimenezi sitikuvulazani." Chikhamu cha anthu chija chinapitirizabe kukuwa. "Matigari! Matigari!" Amene ankatsogolera gulu la asilikali anadzakhuthulidwa m'malole aja anayamba kuchenjeza anthu aja. "Amene atayere- keze kukuwanso awomberedwa." Chifukwa cha mantha, anthu aja anakhala chete, koma sikuti panali bata lenileni pamalowa. Panali chinam'balala chifukwa ambiri ankachita chidwi kuti aone zomwe zitachitike. 258