Matigari
"Anduna!" Matigari anaitokosa motero nkhani. "Pajatu ndi-
nakufunsani funso koma simunandiyankhe. Mwina ndichite
molibwerezanso. Kodi ndi kuti m'dziko lino kumene munthu
amene wadzimanga ndi lamba wamtendere angapeze choonadi
ndi chilungamo?"
Nduna ija inachita chibwibwi. Inkaoneka kuti sinakonzeke
kuti Matigari aifunsaso funsolo. Kenako inatembenukira kwa
anthu anali muholomo.
"Munthu ameneyu yemwe akumadzitchula kuti ndi Matiga-
ri ma Njiruungi akuyenera kunyongedwa. Kodi simunamve
pamene amavomereza yekha kuti anapha anthu? Koma oweru-
za athu amupeza kuti ndi wopenga. Wofufuza milandu wovala
chipewa choonetsa maso okha uja anavomereza kuti Matigari
anagawira anzake onse omwe anamangidwa nawo, buledi
komanso mowa potengera zimene Yesu anachita pa Mgonero
wa Ambuye. Nokhanso munamumva apa akubwebwetuka kuti
wakhala m'nkhalango komanso m'mapiri kwa zaka zambiri
akumenyana ndi Boy komanso Williams. Zonsezi
zikungosonyezeratu kuti munthuyudi ndi wozerezeka. Major
Howard Williams ndi John Boy anapita kukamenyana ndi
zigawenga pa nthawi yomwe nkhondo yomenyera ufulu
inkachitika, mwina titero kunena kwake kuti mumvetse.
Zimamveka kuti anafa pamene ankamenyana ndi zigawengazo.
Anthu awiri amenewa anapatsidwa mamendulo aulemu
chifukwa cha kulimba mtima kwawo komanso mtima wawo
wololera kufera ena: A Williams anapatsidwa CBE
(Commander of the British Empire), ndipo Boy anapatsidwa
MBE (Member of the Order of the British Empire). Komano
taganizani, kodi mukuganiza kuti munthu amene mutu wake
ukugwira ntchito bwinobwino angabwere pagulu pano
196