Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 196
Matigari
amenewa ndi amene amayambitsa mpungwepungwe komanso
magawano m'dziko muno. Ndi anthu ngati omwewa amene
akuchititsa kuti asilikali ayambe kugalukira boma. Funso limene
anafunsa lija likusonyeza kuti mawaya ena a m'mutu mwake
anaduka, mutu wake sukoka. Choncho oweruza athu agamula
kuti apititsidwe kuchipatala cha anthu amisala kuti akaone nga-
ti mutu wake ukuyenda bwinobwino . . . Ndiye mwaonatu, og-
wira ntchitonu mumatsogoleredwa ndi munthu waziwala
m'maso."
Asanatulutsidwe panja, Ngaruro wa Kiriro anakuwa kuti:
"Mukhoza kundimanga ineyo, koma dziwani kuti ogwira ntchi-
to sadzaleka kumenyera nkhondo ufulu wawo!"
Poyankha nduna ija inati: "Mwaona mmene maganizo
opotoka angasocheretsere munthu!"
Kenako nduna ija inatembenukira kwa Matigari ma Njiruun-
gi. Matigari anali ataima nji ngati chitsa chotsala mulupsa ndipo
ankangooneka ngati chiphona. Iye sankatekeseka mpang'ono
pomwe. Ndi khalidwe limeneli limene linkachititsa kuti anthu
azimuopa. Ankayang'ana ndi diso lachiweruzo, diso lokhala
ngati mpeni. Ndipo akamayang'ana munthu ankakhala ngati
akumuona ndi matumbo omwe. Nduna ija sinkayang'anana ndi
Matigari maso ndi maso. Kenako inayamba kuchita zinthu
mokayikakayika ndipo zinayamba kukhalanso ngati yataya
lilime lake moti pamene inali mkati molifunafuna, Matigari ana-
pezerapo mpata woyankhula.
Tsopano zinkangokhala ngati asinthana mbali. Iyeyo
anayamba kuchita zinthu ngati ndi amene ali Nduna Yoona
Zachilungamo ndipo ndunayo inkakhala ngati ikuuzidwa chi-
gamulo.
195