Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 198
Matigari
n'kumadzitama kuti anapha anthu? Ndiponso mafunso amene
akufunsawa, kodi angatuluke pakamwa pa anthu omwe pakati
pa mapewa awo pali mitu yabwinobwino ngati wa ine komanso
yanuyo? Oweruza athu aona kuti mutu wa munthu ameneyu
ndi wosukusa ndipo akuyenera kupititsidwa kuchipatala cha
anthu amisala. Akapita kumeneko akaikidwa pamalo achitetezo
chokhwima kwambiri, chifukwa ndi munthu woopsa komanso
ali ndi maganizo aupandu m'mutu mwakemu."
Kenako Matigari anatembenuka mwadzidzidzi moyang'ana
Nduna Yoona Zachilungamo ija, mkulu wa apolisi, oweruza aja,
bwanamkubwa uja, wansembe, Boy, Williams, pulofesa wokha-
zikika wa Parro to lo gy komanso alendo ena onse olemekezeka
omwe anali kutsogolo kuja.
Iye anayamba kuonekanso wachinyamata ndipo mawu ake
anayamba kumveka ngati chiphaliwali.
"Nyumba ija ndi yanga chifukwa ndinaimanga ndi manja
anga. Mindanso ndi yanga chifukwa ndine ndinailima.
Mafakitalenso ndi anga chifukwa ndinawamanga komanso
ndinkagwirako ntchito. Sindidzasiya kumenya nkhondo kuti
mundibwezere zinthu zimenezi. Ndinakhetsa magazi popanga
zinthu zimenezi ndipo sindingawakhetse pachabe. Tsiku lina
minda idzabwerera kwa mwini wake mlimi, komanso chuma
cha m'dzikoli chidzabwerera kwa amene amachipanga.
Umphawi komanso mavuto ayenera kudzathetsedwa m'dziko
lathu lino!"
Kenako Matigari analoza Robert Williams ndi John Boy ngati
mmene amachitira munthu amene akukalipira mwana.
"Ndiponso iweyo munthu wankhanza komanso wantchito
wakoyo, ndiponso zidole zanu zonsezi, izi zili kutsogolo kuno,
ndikunena ndunayi, akuluakulu a apolisi, akuluakulu a asilikali,
197