Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 58
Sewero la Mfumu Edipa
omwe panakumana misewu itatu.
Zimenezi zinachititsa kuti Edipa ayambe kuda nkhawa kwambiri.
Iye anakumbukira kuti anapha munthu pamene ankathawa kwawo ku
Korinto kuti ulosi wofanana ndi womwewu usakwaniritsidwe. Iye ana-
thawa kwawo atawuzidwa kuti adzapha bambo ake n’kukwatira mayi
ake. Pa nthawiyi nthenga wina wachikulire anatulukira kuchokera ku
Korinto ndipo anabwera ndi uthenga wakuti bambo Edipa, a Polebasi
omwe ndi mfumu ya kumeneko, amwalira. Iye akuwuza Edipa kuti pa-
mene bambo akewo amamwalira ananena kuti Edipa ndi amene akuye-
nera kukhala mfumu yotsatira. Koma Edipa akukana kubwerera ku Ko-
rinto chifukwa choti mayi ake adakali moyo. Iye akulumbira kuti sadza-
bwerera kwawo pokhapokha mayi akewonso adzamwalire. Koma pofu-
na kumukhazika mtima pansi, nthengayo akumufotokozera kuti a Pole-
basi si bambo ake omubereka komanso kuti Merope si mayi ake enieni.
Akumuwuzanso kuti iyeyo ndi amene anamutola kuphiri atatayidwa.
Edipa akuzindikira kuti mawu amenewa akufanana kwambiri ndi ame-
ne m’busa wankhosa anayitanidwa ndi Yokasi uja ananena. Zimenezi
zikutsimikizira kuti ulosi wakale kwambiriwo wakwaniritsidwa m’njira
yochititsa mantha kwambiri. Yokasi atazindikira kuti anakwatira ndi
mwana wake anakalowa kuchipinda kwake n’kukadzimangirira ndipo
Edipa nayenso anadzikolowola maso kuti asawonenso chilichonse.
Kenako anadzipatsa chilango chothamangitsidwa ku Thebesi chomwe
analonjeza kuti adzachipereka kwa aliyense amene angadzapezeke kuti
ndi amene anapha Mfumu Layasi.
53