Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 57
Sewero la Mfumu Edipa
KUZUKUTA MWACHIDULE ZOCHITIKA M’SEWEROLI
Zaka khumi ndi ziwiri zochitika za m’seweroli zisanachitike, Edipa ana
longedwa kukhala mfumu ya ku Thebesi atachita zakupsa populumutsa
anthu a mumzindawu kuchokera kwa chilombo china chomwe chinayi-
ma pachipata cholowera mumzindawu. Chilombochi chinkadya anthu
moti palibe ankalowa kapena kutuluka mumzindawu. Chilombochi
chinathawa pamalowa n’kukadzipha Edipa atayankha molondola ndagi
yomwe chilombocho chinkapereka. Ndiye popeza mfumu Layasi yo-
mwe inkalamulira Thebesi inali itangophedwa kumene, anthu analonga
Edipa kukhala mfumu yawo chifukwa chowapulumutsa. Anamupatsa-
nso Yokasi, yemwe anali mkazi wa mfumuyo kuti akhale mkazi wake.
Ndiye tsopano, mliri winanso wowopsa kwambiri unabuka ku
Thebesi ndipo anthu anapita kwa Edipa kukamupempha kuti awapulu-
mutsenso ku mliriwo ngati mmene anachitira ulendo wapita. Mfumuyo
inkawoneka kuti yamvetsa vuto lawo. Ndiyeno Kireyo, mchimwene wa
mkazi wake Yokasi, anatulukira kuchokera ku Defi komwe anakafunsira
kwa mulungu wina dzina lake Apolo. Mulunguyo anawawuza kuti
zinthu zikhoza kuyambanso kuyenda bwino ngati munthu amene ana-
pha Mfumu Layasi atathamangitsidwa mumzindawo.
Poyesayesa kupeza anthu amene anapha mfumuyo, Edipa anayita-
nitsa wolosera wina dzina lake, Teresi. Teresi anakana kuwuza mfumu-
yo zimene anawona, koma mfumuyo inayamba kumuwumiriza kuti
anene chilungamo chokhachokha ndipo iye anawuza Edipa kuti iyeyo
ndi amene anapha Mfumu Layasi. Edipa anakwiya kwambiri ndi mawu
amenewa moti anayamba kuyimba mlandu Kireyo, mlamu wake uja,
kuti ndi amene wagwirizana ndi Teresi kuti adzanene bodza n’cholinga
choti alande ufumu. Pa nthawiyi mpamene Yokasi anatulukira ndipo
anawuza mwamuna wakeyo kuti olosera ndi anthu achinyengo koma-
nso osathandiza. Pofuna kumutsimikizira mfundo imeneyi, anamufoto-
kozera za ulosi wina womwe unkanena kuti mwana yemwe Yokasiyo
adzabereke adzapha bambo ake n’kukwatira ndi mayi ake. Pofuna ku-
mutambasulira bodza lokhudza ulosiwo, anawuza Edipa kuti mwa nayo
anaphedwa n’kukatayidwa kumapiri komanso kuti mwamuna wake
Layasi anaphedwa ndi achifwamba patapita zaka zambiri, pamalo ena
52