Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 96
Paphata pa Chichewa
Khuta mavuto: Kutopa ndi mavuto.
Chitsanzo: Anthu ambiri amene amadzikhweza amakhala
oti akhuta mavuto.
Khutaufe: Kudya zomwe zatsala kuti kenako ufe.
Chitsanzo: Chakudya chomwe tatsala nacho ndi khutaufe.
Khutchakhutcha:
(a) Mawuwa amanenedwa ngati munthu wonenepa
kapena wamkulu akuvina kapena kuyenda movutikira.
Chitsanzo: (1) Ndinakumana nawo ali khutchakhutcha. (2)
Povina amachita kuti khutchakhutcha.
Khutu limodzi: Kumva pang’ono.
Chitsanzo: Nkhaniyo ndinaimva ndi khutu limodzi.
Khutula phutula: Kuyesetsa kuyenda uku ndi uku kuti
upeze thandizo.
Chitsanzo: Atazingwa, amangoti khutula phukula,
kusakasaka woti awathandize.
Khuzumuka: Mawu amene anthu amanena pouza
munthu wina kuti adekhe, asapupulume.
Chitsanzo: Chonde achimwene khuzumukani.
Khwangwala: Munthu wamantha.
Chitsanzo: Inutu ndi khwangwala, kumangochita mantha
ndi chilichonse!
Khwasukhwasu:
(s) Kuyenda osatenga kanthu kumanja.
Chitsanzo: Amangoyenda khwasukhwasu pobwera kuno.
(b) Ndiwo zanyama.
Chitsanzo: Madzulo ano tidyera khwasukhwasu.
95