Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 95
Paphata pa Chichewa
Khope: Kuchita mwayi kapena kuuzidwa kuti uchite
zomwe umafuna kale. Khope ndi mbalame imene
imakonda kuulukira kumene kukupita mphepo. Mawuwa
amagwira ntchito ponena za munthu amene watumidwa
chinachake, iyenso ali ndi zochita zina komweko, moti
popita sanyinyirika.
Chitsanzo: Ndimadabwa kuti anasangalala kwambiri
nditamutuma kupita kumeneku. Sindimadziwa kuti
ndikutumiza khope.
Khuluku: Mawu obwerekera kuchingerezi onena za mun-
thu wosadalirika komanso wopanda pake.
Chitsanzo: Bamboyu ndi khuluku.
Khumata: Khala mwamantha.
Chitsanzo: Ukufuna anawa azikhala mokhumata chifukwa
cha iwe!
Khumbi: Kanyumba komwe anthu amamanga kumunda
kuti azindikirira apusi kapena nyama zina zomwe zinga-
wadyere mbewu zawo. Amagwiritsanso ntchito kanyumba-
ka popuma akatopa ndi kulimba ndiponso amasungamo
zinthu zina.
Chitsanzo: Mukamaliza mundipeza kukhumbi.
Khumbira: Kusirira, kufuna chinachake kwambiri.
Chitsanzo: Mtsikana uja ndimamukhumbira.
Khumucha: Munthu wolemera.
Chitsanzo: M’dala amene uja ndi khumucha.
Khumudwa: Kusakondwa.
Chitsanzo: Ataona kuti nsima yake yadyedwa,
anakhumudwa kwambiri.
94