Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 55
Paphata pa Chichewa
padzaphuka kanthu.
Dzala:
(a) Munthu wodya kwambiri komanso mosasankha.
Chitsanzo: Pakamwa pawo ndi padzala.
(b) Munthu yemwe amangomupatsa zinthu zakutha.
Chitsanzo: Ifetu ndiye ndi dzala, amatipatsa chinthu
chikatha.
Dzandidzandi: Kuyenda mosakhazikika ngati ukufuna
kugwa. Nthawi zina munthu amayenda chonchi ngati
waledzera.
Chitsanzo: (1) Atasenza thumbalo anayamba kuyenda
mwadzandidzandi. (2) Ndinakumana nawo ali
dzandidzandi.
Dzanja lasefa: Dzanja losasunga ndalama.
Chitsanzo: M’tauni muno ukhoza kutuwa koopsa ngati
utakhala ndi dzanja la sefa.
Dzanja limodzi: Ndekha, yekha, okha.
Chitsanzo: (1) Ukamalima munda waukulu umafunika
kukhala ndi aganyu, osati dzanja limodzi. (2) Dzanja
limodzi lingakwanitse bwanji kuchita zonsezi?
Dzaoneni: Chinthu ngati chafika poipa kapena chakula
kwambiri timati chafika padzaoneni. Angatanthauzenso
zinthu zochuluka.
Chitsanzo: (1) Ali ndi ndalama zadzaoneni. (2) Ali pa
umphawi wadzaoneni.
Dzera kunkhongo: Kusadziwa zinazake, kusazindikira
kodabwa.
Chitsanzo: Ndinenapo bwanji maganizo anga popeza
54