Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 54

Paphata pa Chichewa Dyetsa njomba: (a) Kuchita zosakhulupirika, kupusitsa munthu. Chitsanzo: Si kale pamene anayamba kuwadyetsa njomba akazi awo aja. (b) Kubwiza, kupusitsa munthu mumpira. Chitsanzo: Anadyetsa njomba n’kugoletsa. Dyokodyoko: Kufunitsitsa kumva kapena kuchita zinazake. Chitsanzo: Anzanu mitima ikungoti dyokodyoko, tatiuzeni! Dyokodyoko: Kufunitsitsa zinazake. Chitsanzo: Mtima wanga umangoti dyokodyoko nditaona ndalamazo. Dyola: Kunyengereredwa komanso kutamidwa. Chitsanzo: Anazolowera dyola. Dyoo: Kungokhala ndwii. Chitsanzo: Akakhala kuti sanamwe mowa amangoti dyoo. Dyoo: Kupusa. Chitsanzo: Tamuonani, ali dyoo! Dzadzada: (a) Kutema, kumenya. Chitsanzo: Anzake amudzadzada ndi chikwanje. (b) Kuphwanya. Chitsanzo: Tadzadzadani ndiwoyi. Dzala madzi: Chita mantha. Chitsanzo: Titangomva kulira kwa mfuti, tonse tinadzala madzi. Dzala ufa: Kunena bodza. Chitsanzo: Ukhoza kudzala ufa, koma usaganize kuti 53